Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 39:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anatsika naye Yosefe kunka ku Aigupto; ndipo Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda, Maigupto, anamgula iye m'manja mwa Aismayeli amene anatsika naye kunka iumeneko.

2. Ndipo Yehova anali ndi Yosefe; ndipo iye anali wolemeralemera; nakhala m'nyumba ya mbuyace M-aigupto.

3. Ndipo mbuyace anaona kuti Yehova anali ndi iye, ndi kuti Yehova anamlemereza m'dzanja lace zonse anazicita.

4. Ndipo Yosefe anapeza ufulu pamaso pace, ndipo anamtumikira iye; ndipo anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yace, naika m'manja mwace zonse anali nazo.

5. Ndipo panali ciyambire anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yace, ndi pa zace zonse, Yehova anadalitsa nyumba ya M-aigupto cifukwa ca Yosefe; ndipo mdalitso wa Yehova unali pa zace zonse, m'nyumba ndi m'munda.

Werengani mutu wathunthu Genesis 39