Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 38:18-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo iye anati, Cikole canji ndidzakupatsa iwe? Ndipo mkazi anati, Mphete yako, ndi cingwe cako, ndi ndodo iri m'dzanja lako. Ndipo anampatsa izo, nalowana naye, ndipo mkazi anatenga pakati ndi iye.

19. Ndipo mkazi anauka nacoka, nabvula copfunda cace, nabvala zobvala zamasiye zace.

20. Ndipo Yuda anatumiza kamwana ka mbuzi ndi dzanja la bwenzi lace Madulami, kuti alandire cikole pa dzanja la mkazi; koma sanampeza iye.

21. Ndipo anafunsa amuna a pamenepo kuti, Ali kuti wadama uja anali pambali pa njira pa Enaimu? ndipo iwo anati, Panalibe wadama pano.

22. Ndipo iye anabwera kwa Yuda nati, Sitinampeza mkazi; ndiponso amuna a pamenepo anati, Panalibe wadama pano.

23. Ndipo Yuda anati, Azilandire kuti tingacitidwe manyazi: taona, ndinatumiza mwana uyu wa mbuzi, ndipo sunampeza iye.

24. Ndipo panali itapita miyezi itatu, anamuuza Yuda kuti, Tamara mpongozi wako wacita cigololo, ndiponso taonani, ali ndi pakati ndi cigololoco. Ndipo Yuda anati, Mturutse iye kuti amponye pamoto.

25. Pamene anamturutsa Iye, mkazi anatumiza kwa mpongozi wace kuti, Ndi mwamuna mwini izi ndatenga pakati; ndipo mkazi anati, Tayang'anatu, za yani zimenezi, mphete, ndi cingwe, ndi ndodo?

26. Ndipo Yuda anabvomereza nati, Akhale wolungama wopambana ine, cifukwa ine sindinampatsa iye Sela mwana wanga wamwamuna. Ndipo iye sanamdziwanso mkaziyo.

27. Ndipo panali nthawi ya kubala kwace, taonani, amapasa anali m'mimba mwace.

28. Ndipo panali pamene anabala kuti mmodzi anaturutsa dzanja; ndipo namwino anatenga cingwe cofiira namanga pa dzanja lace, kuti, Uyu anayamba kubadwa.

29. Ndipo panali pamene iye ana bweza dzanja lace, kuti, taona, mbale wace anabadwa, ndipo namwino anati, Wadziposolera wekha bwanji? cifukwa cace dzina lace linachedwa Pereze.

30. Ndipo pambuyo pace anabadwa mbale wace, amene anali ndi cingwe cofiira pamkono pace, dzina lace linachedwa Zera.

Werengani mutu wathunthu Genesis 38