Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 37:29-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Ndipo Rubeni anabwera kudzenje, ndipo taonani, Yosefe mulibe m'dzenjemo: ndipo iye anang'amba nsaru yace.

30. Ndipo anabwera kwa abale ace, nati, Mwana palibe; ndipo ine ndipita kuti?

31. Ndipo anatenga malaya ace a Yosefe, napha tonde, nabvika malaya m'mwazi wace:

32. natumiza malaya amwinjiro, nadza nao kwa atate ao: ndipo anati, Siwa tawatola; muzindikire tsono ngati ndi malaya a mwana wanu, kapena ndi ena.

33. Ndipo anazindikira nati, Ndiwo malaya a mwana wanga: wajiwa ndi cirombo: Yosefe wakadzulidwa ndithu.

34. Yakobo ndipo anang'amba malaya ace, nabvala ciguduli m'cuuno mwace namlirira mwana wace masiku ambiri.

35. Ndipo ana amuna ace onse ndi ana akazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndirinkulirabe. Atate wace ndipo anamlirira.

36. Amidyani ndipo anamgulitsa iye anke ku Aigupto kwa Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda.

Werengani mutu wathunthu Genesis 37