Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 34:21-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Anthu amenewa ali amtendere pamodzi ndi ife; cifukwa cace akhale m'dzikomo, acite malonda m'menemo: pakuti taonani dzikololirilalikurulokwaniraiwo; tidzitengere ana ao akazi akhale akazi athu, tiwapatse amenewa ana athu akazi.

22. Anthuwo adzatiloleza ife tikhale nao anthu amodzi, pokhapo amuna onse a mwa ife adzadulidwa, monga iwo adulidwa.

23. Kodi ng'ombe zao ndi cuma cao ndi zoweta zao sizidzakhala zathu? Pokhapo tibvomerezana nao ndipo adzakhala pamodzi ndi ife.

24. Ndipo onse amene anaturuka pa cipata ca mudzi wao anamvera Hamori ndi mwana wace Sekemu, nadulidwa amuna onse akuturuka pa cipata ca mudzi wao.

25. Ndipo panali tsiku lacitatu pamene anamva kuwawa, ana amuna awiri a Yakobo, Simeoni ndi Levi, abale ace a Dina, anatenga wina lupanga lace wina lace, nalimbika mtima nalowa m'mudzi napha amuna onse.

26. Ndipo anapha Hamori ndi Sekemu mwana wace ndi lupanga, naturutsa Dina m'nyumba ya Sekemu nacoka naye.

27. Ndipo ana amuna a Yakobo anadzakwa ophedwa nafunkhamudzi cifukwa anamuipitsa mlongo wao.

28. Ndipo analanda nkhosa zao ndi zoweta zao ndi aburu ao, ndi za m'mudzi, ndi za m'munda;

29. ndi cuma cao conse ndi ana ao ndi akazi ao anawagwira, nafunkha zonse za m'nyumba.

30. Ndipo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, Mwaodisautsa ndi kundinunkhitsa ine mwa anthu okhala m'dzikomu, mwa Akanani ndi mwa Aperezi; ndipo ine ndine wa anthu owerengeka, adzandisonkhanira ine ndi kundikantha: ndipo ndidzapasulidwa ine ndi a pa nyumba yanga.

Werengani mutu wathunthu Genesis 34