Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 34:11-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo Sekemu anati kwa atate wace wa mkazi ndi kwa abale ace, Tipeze ufulu pamaso panu, cimene mudzanena kwa ine ndidzapereka.

12. Mundipemphe ine za mitulo ndi zaulere zambirimbiri, ndipo ndidzapereka monga mudzanena kwa ine; koma mundipatse ine namwaliyo akhale mkazi wanga.

13. Ndipo ana ace amuna a Yakobo anayankha Sekemu ndi Hamori atate wace monyenga, nanena, popeza anamuipitsa Dina mlongo wao,

14. nati kwa iwo, Sitingathe kucita ici, kupereka mlongo wathu kwa mwamuna wosadulidwa; cifukwa kumeneko ndiko kuticepetsa ife.

15. Koma apa pokha tidzakubvomerezani: ngati mudzakhala onga ife ndi kudulidwa amuna onse;

16. pamenepo tidzakupatsani inu ana athu akazi, ndipo tidzadzitengera ana anu akazi, ndipo tidzakhala pamodzi ndi inu, ndi kukhala mtundu umodzi.

17. Koma mukapanda kutimvera ndi kusadulidwa, pamenepo tidzatenga mwana wathu wamkazi, ndi kumuka naye.

18. Mau ao ndipo anakomera Hamori ndi Sekemu mwana wace wa Hamori.

19. Ndipo mnyamatayo sanacedwa kucicita popeza anakondwera ndi mwana wace wamkazi wa Yakobo; ndipo iye anali wolemekezedwa woposa onse a pa banja la atate wace.

20. Ndipo Hamori ndi Sekemu mwana wace anafika ku cipata ca mudzi wao, nalankhulana ndi anthu a mudzi wao, kuti,

21. Anthu amenewa ali amtendere pamodzi ndi ife; cifukwa cace akhale m'dzikomo, acite malonda m'menemo: pakuti taonani dzikololirilalikurulokwaniraiwo; tidzitengere ana ao akazi akhale akazi athu, tiwapatse amenewa ana athu akazi.

22. Anthuwo adzatiloleza ife tikhale nao anthu amodzi, pokhapo amuna onse a mwa ife adzadulidwa, monga iwo adulidwa.

23. Kodi ng'ombe zao ndi cuma cao ndi zoweta zao sizidzakhala zathu? Pokhapo tibvomerezana nao ndipo adzakhala pamodzi ndi ife.

24. Ndipo onse amene anaturuka pa cipata ca mudzi wao anamvera Hamori ndi mwana wace Sekemu, nadulidwa amuna onse akuturuka pa cipata ca mudzi wao.

25. Ndipo panali tsiku lacitatu pamene anamva kuwawa, ana amuna awiri a Yakobo, Simeoni ndi Levi, abale ace a Dina, anatenga wina lupanga lace wina lace, nalimbika mtima nalowa m'mudzi napha amuna onse.

26. Ndipo anapha Hamori ndi Sekemu mwana wace ndi lupanga, naturutsa Dina m'nyumba ya Sekemu nacoka naye.

27. Ndipo ana amuna a Yakobo anadzakwa ophedwa nafunkhamudzi cifukwa anamuipitsa mlongo wao.

Werengani mutu wathunthu Genesis 34