Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 34:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Dina mwana wamkazi wa Leya, amene anambalira Yakobo, ananka kukaona akazi a kumeneko.

2. Pamene anamuona iye Sekemu, mwana wace wamwamuna wa Hamori Mhivi, karonga wa dzikolo, anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa,

3. Ndipo mtima wace unakhumba Dina mwana wace wamkazi wa Yakobo, ndipo anamkonda namwaliyo, nanena momkopa namwaliyo.

4. Ndipo anati Sekemu kwa atate wace Hamori kuti, Munditengere ine mkazi uyo akhale mkazi wanga.

5. Ndipo anamva Yakobo kuti anamuipitsa Dina, mwana wace wamkazi; ana ace amuna anali ndi zoweta zace kudambo: ndipo Yakobo anakhala cete mpaka anafika iwo.

6. Ndipo Hamori atate wace wa Sekemu anaturuka kunka kwa Yakobo kukanena ndi iye.

7. Ndipo pakumva ico ana ace amuna a Yakobo anabwera pocokera kudambo: amunawo ndipo anaphwetekwa mtima, nakwiya kwambiri, cifukwa iyeyo anacita copusa coipira Israyeli pakugona ndi mwana wamkazi wa Yakobo; ndico cosayenera kucita.

8. Ndipo Hamori ananena ndi iwo, kuti, Mtima wa Sekemu mwana wanga umkhumba mwana wako wamkazi: umpatsetu kuti akhale mkazi wace.

9. Mukwatirane ndi ife: tipatseni ife ana anu akazi, ndiponso dzitengereni ana athu akazi.

10. Ndipo mudzakhala pamodzi ndi ife, dziko lidzakhala pamaso panu; khalani m'menemo ndi kucita malonda, ndi kukhala nazo zanuzanu m'menemo.

Werengani mutu wathunthu Genesis 34