Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 33:12-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo Esau anati, Tiyeni timuke; nditsogolera ndine.

13. Ndipo anati kwa iye, Mbuyanga adziwa kuti ana ali ambowa, ndipo nkhosa ndi zoweta ndiri nazo zirinkuyamwitsa: ndipo akathamangitsa tsiku limodzi zoweta zonse zidzafa.

14. Mbuyanga atsogoleretu kapolo wace, ndipo ine ndidzazitsogolera pango'no-pang'ono monga mwa mayendedwe a zoweta ziri pamaso panga, ndi monga mwa mayendedwe a ana, mpaka ndifike kwa mbuyanga ku Seiri.

15. Ndipo Esau anati, Ndikusiyire anthu ena amene ali ndi ine, Ndipo iye anati, Cifukwa canji? ndipeze ine ufulu pamaso pa mbuyanga.

16. Ndipo Esau anabwera tsiku lomwelo kunka ku Seiri.

17. Ndipo Yakobo anankabe ulendo wace ku Sukoti, namanga nyumba yace pamenepo, namanga makola a zoweta zace: cifukwa cace dzina lace la kumeneko ndi Sukoti.

18. Ndipo Yakobo anafika ndi mtendere ku mudzi wa Sekemu umene uli m'dziko la Kanani, pamene anacokera ku Padanaramu; namanga tsasa pandunji pa mudzipo.

19. Ndipo anagula ndi ndalama zana limodzi dera la munda kumeneko anamanga bema wace, pa dzanja la ana ace a Hamori atate wace wa Sekemu.

20. Ndipo anamanga pamenepo guwa la nsembe, nacha pamenepo EleloheIsrayeli.

Werengani mutu wathunthu Genesis 33