Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 32:9-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo Yakobo anati, Mulungu wa atate wanga Abrahamu, Mulungu wa atate wanga Isake, Yehova, amene munati kwa ine, Bwera ku dziko lako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakucitira iwe bwino:

10. sindiyenera zazing'ono za zifundo zonse, ndi zoona zonse, zimene mwamcitira kapolo wanu: cifukwa ndi ndodo yanga ndinaoloka pa Yordano uyu; ndipo tsopano ndiri makamu awiri.

11. Mundipulumutsetu ine m'dzanja la mkuru wanga, m'dzanja la Esau; cifukwa ine ndimuopa iye, kapena adzadza kudzandikantha ine, ndi amai pamodzi ndi ana.

12. Ndipo Inu munati. Ndidzakucitira iwe bwino ndithu, ndidzakuyesa mbeu yako monga mcenga wa pa nyanja yaikuru, umene sungathe kuwerengeka cifukwa ca unyinji wace.

13. Ndipo anagona komweko usiku womwewo, natengako zimene anali nazo, mphatso yakupatsa Esau mkuru wace:

14. mbuzi zazikazi mazana awiri, atonde makumi awiri, nkhosa zazikazi mazana awiri, ndi zazimuna makumi awiri,

15. ngamila zamkaka makumi atatu ndi ana ao, ng'ombe zazikazi makumi anai, zazimuna khumi, aburu akazi makumi awiri ndi ana khumi.

16. Ndipo anazipereka zimenezo m'manja a anyamata ace, gulu pa lokha gulu pa lokha: ndipo anati kwa anyamata ace, Taolokani patsogolo panga, tacitani danga pakati pa magulu, tina ndi lina.

17. Ndipo anauza wotsogolera kuti, Pamene akomana nawe mkuru wanga Esau ndi kufunsa iwe kuti, Ndiwe yani, umuka kuti? za yani zimenezi patsogolo pako?

18. pomwepo uziti, Za kapolo wanu Yakobo; ndizo mphatso yotumizidwa kwa mbuyanga Esau; taonani ali pambuyo pathu.

19. Ndipo anauzanso waciwiri ndi wacitatu, ndi onse anatsata magulu, kuti, Muzinena kwa Esau cotero, pamene mukomana naye:

20. ndiponso muziti, Ndiponso, taonani, kapolo wanu Yakobo ali pambuyo pathu, Pakuti anati, Ndidzampembedzera iye ndi mphatso imene ipita patsogolo panga, pambuyo pace ndidzaona nkhope yace; kapena adzandilandira ine.

Werengani mutu wathunthu Genesis 32