Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 31:22-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Tsiku lacitatu anamuuza Labani kuti Yakobo wathawa.

23. Ndipo iye anatenga abale ace pamodzi naye, namlondola iye ulendo wa masiku asanu ndi awiri: nampeza iye pa phiri la Gileadi.

24. Ndipo Mulungu anadza kwa Labani Msuriya usiku, nati kwa iye, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa,

25. Ndipo Labani anakomana naye Yakobo. Ndipo Yakobo anamanga hema wace m'phirimo: ndipo Labani ndi abale ace anamanga m'phiri la Gileadi.

26. Ndipo Labani anati kwa Yakobo, Wacitanji? Wathawa kwa ine mobisika ndi kutenga ana anga akazi, monga mikoli ya lupanga.

27. Wathawanji iwe mobisika, ndi kundicokera kutseri, osandiuza ine, kuti ndikadakumukitsa iwe ndi kusekerera ndi nyimbo ndi lingaka ndi zeze?

28. Ndipo sunandiloleza ine ndimpsompsone ana anga amuna ndi akazi? wapusa iwe pakucita cotero.

29. M'dzanja langa muli mphamvu yakucitira iwe zoipa koma Mulungu wa atate wako anati kwa ine usiku walero, kuti, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.

30. Tsono ungakhale ukadamuka cifukwa mtima wako ulinkukhumba nyumba ya atate wako, bwanji waba iwe milungu yanga?

31. Ndipo anayankha Yakobo nati kwa Labani, Cifukwa ndinaopa: cifukwa kuti, ndinati, Kapena udzandilanda ine ana ako akazi.

32. Ali yense umpeza ali nayo milungu yako, asakhale ndi movo: pamaso pa abale athu, tayang'anira zako ziri ndi ine, nuzitenge wekha. Pakuti sanadziwe Yakobo kuti Rakele anaiba.

33. Ndipo Labani analowa m'hema wa Yakobo, ndi m'hema wa Leya, ndi m'mahema a adzakazi awiri aja; koma sanapeze, Ndipo anaturuka m'hema wa Leya nalowa m'hema wa Rakele.

34. Ndipo Rakele anatenga aterafiwo nabisa pa cokhalira ca ngamila, nakhala pamenepo, Ndipo Labani anafunafuna m'hema monse, koma sanawapeze.

35. Ndipo Rakele anati kwa atate wace, Asakwiye mbuyanga kuti sindingathe kuuka pamaso panu; cifukwa zocitika pa akazi ziri pa ine. Ndipo Labani anafunafuna koma sanapeze aterafiwo.

36. Ndipo anakwiya Yakobo namkalipira Labani: ndipo Yakobo anayankha nati kwa Labani, Kodi ndacimwa ciani? ucimo wanga nguti, kuti unanditsatatsata ine pambuyo panga?

37. Pakuti wafunafuna monse ndiri nazo, kodi wapeza ciani pa zinthu za m'nyumba mwako? Tafika naco apa pa abale anga ndi ako, kuti aweruze pa ife tonse awiri.

38. Zaka makumi awiriwo ndakhala nawe, nkhosa ndi mbuzi zako zazikazi sizinapoloze, ndi abira a zoweta zako sindinadye.

39. Cimene cinazomoledwa ndi cirombo sindinacitengere kwa iwe; ndekha ndinalipira; pa dzanja langa unacifuna, cingakhale cobedwa kapena pausiku kapena pausana.

Werengani mutu wathunthu Genesis 31