Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 31:1-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yakobo afuna kwao nathawa nazo zace, Ndipo anamva mau a ana ace a Labani kuti, Yakobo watenga zonse za atate wathu; m'zinthu zinali za atate wathu wapeza iye cuma ici conse.

2. Ndipo Yakobo anaona nkhope ya Labani, taonani, siinamuonekera iye monga kale.

3. Ndipo Yehova anati kwa Yakobo, Bwera ku dziko la atate wako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakhala ndi iwe.

4. Ndipo Yakobo anatumiza naitana Rakele ndi Leya adze kubusa ku zoweta zace,

5. ndipo anati kwa iwo, Ndiona ine nkhope ya atate wanu kuti siindionekera ine monga kale; koma Mulungu wa atate wanga anali ndi ine.

6. Ndipo inu mudziwa kuti ndi mphamvu zanga zonse ndatumikira atate wanu.

7. Ndipo atate wanu wandinyenga ine, nasinthanitsa malipilo anga kakhumi; koma Mulungu sanamlole iye andicitire ine coipa.

8. Akati cotero, Zamathotho-mathotho zidzakhala malipilo ako, zoweta zonse zinabala zamathotho-mathotho; ndipo akati iye cotere, Zamipyololo-mipyololo zidzakhala malipilo ako, ziweto zonse zinabala mipyololo-mipyololo.

9. Comweco Mulungu anazicotsa zoweta za atate wanu, nandipatsa ine.

10. Ndipo panali potenga mabere ziwetozo, ine ndinatukula maso anga, ndipo ndinapenya m'kulota, taonani, atonde okwera ziweto anali amipyololo-mipyololo, amathotho-mathotho, ndi amaanga-maanga.

11. Mthenga wa Mulungu ndipo anati kwa ine m'kulotamo, Yakobo; nati ine, Ndine pano,

12. Ndipo anati, Tukulatu maso ako, nuone, atonde onse amene akwera zoweta ali amipyololo-mipyololo, amathotho-mathotho, ndi amaangamaanga: cifukwa ndaona zonse zimene Labani akucitira iwe.

13. Ine ndine Mulungu wa ku Beteli, kuja unathira mafuta pamwala paja, pamene unandilumbirira ine cilumbiriro: tsopano uka, nucoke m'dziko lino, nubwerere ku dziko la abale ako.

14. Ndipo Rakele ndi Leya anayankha, nati kwa iye, Kodi tiri nalonso gawo kapena colowa m'nyumba ya atate wathu?

15. Kodi satiyesa ife alendo? cifukwa anatigulitsa ife, nathanso kuononga ndalama zathu.

16. Cifukwa kuti cuma conse Mulungu anacicotsa kwa atate wathu ndi cathu ndi ca ana athu; tsono, zonse wakunenera iwe Mulungu, ucite.

Werengani mutu wathunthu Genesis 31