Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 30:37-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

37. Ndipo Yakobo anatenga nthyole za mtengo wowisi walibne, ndi za mtengo wakatungurume, ndi za mtengo waarimoni, nakupula m'menemo mizere yoyera, naonetsa moyera mwa m'nthyolemo.

38. Ndipo anaimitsa nthyole zimene anazikupula pandunji ndi zoweta m'micera yakumwera, m'mene ziweto zinafika kumweramo, ndipo zidatenga mabere pamene zinadza kumwa.

39. Ndipo ziweto zinatenga mabere patsogolo pa nthyolezo, ndipo zoweta zinabala zamipyololomipyololo, ndi mathotho-mathotho, ndi zamaanga-maanga.

40. Ndipo Yakobo analekanitsa ana a nkhosa naziika nkhope za zoweta kuti ziyang'anire zamipyololo-mipyololo, ndi zakuda zonse za m'zoweta za Labani, ndipo anaika magulu ace pa okha; sanaziika pa zoweta za Labani.

41. Ndipo panali pamene zoweta zolimba zidatenga mabere, Yakobo anaika nthyole pamaso pa zoweta m'miceramo kuti zitenge mabere pa nthyolezo.

42. Koma pamene ziweto zinali zofoka, sanaziika zimenezo: ndipo zofoka zinali za Labani, ndi zolimba zinali za Yakobo.

43. Munthuyo ndipo anakula kwambiri, nali nazo zoweta zambiri, ndi akapolo amuna ndi akazi, ndi ngamila, ndi aburu.

Werengani mutu wathunthu Genesis 30