Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 30:10-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo Zilipa mdzakazi wace wa Leya anambalira Yakobo mwana wamwamuna.

11. Ndipo Leyaanati, Wamwai ine! ndipo anamucha dzina lace Gadi.

12. Ndipo Zilipa mdzakazi wa Leya anambalira Yakobo mwana wamwamuna waciwiri.

13. Ndipo Leya anati, Ndakondwa inel cifukwa kuti ana akazi adzandicha ine wokondwa: ndipo anamucha dzina lace Aseri.

14. Ndipo Rubeni ananka masiku akudula tirigu, napeza zipatso za mankhwala a cikondi m'thengo, nazitengera kwa amace Leva, Ndipo Rakele anati kwa Leya, Undipatseko mankhwala a mwana wako.

15. Ndipo iye anati kwa Rakele, Kodi mpacabe kuti iwe wacotsa mwamuna wanga? Kodi ufuna kucotsanso mankhwala a mwana wanga? Rakele ndipo anati, Cifukwa cace iye adaagona nawe usiku uno cifukwa ca mankhwala a mwana wako.

16. Ndipo Yakobo anadza madzulo kucokera kumunda, ndipo Leya ananka kukomana naye, nati, Ulowe kwa ine cifukwa ndakulipilira iwe ndi mankhwala a mwana wanga. Ndipo anagona naye usiku womwewo.

17. Ndipo Mulungu anamvera Leya, ndipo anatenga pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna wacisanu.

Werengani mutu wathunthu Genesis 30