Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 30:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamene Rakele anaona kuti sanambalira Yakobo ana, Rakele anamcitira mkuru wace nsanje; nati kwa Yakobo, Ndipatse ana ndingafe.

2. Ndipo Yakobo anapsa mtima ndi Rakele; nati, Kodi ine ndikhala m'malo a Mulungu amene akukaniza iwe zipatso za mimba?

3. Ndipo Rakele anati, Taonani mdzakazi wanga Biliha, mulowe kwa iye; ndipo iye adzabala pa maondo anga, kuti inenso ndionerepo ana pa iye.

4. Ndipo Rakele anampatsa iye Biliha mdzakazi wace akhale mkazi wace; ndipo Yakobo analowa kwa iye.

5. Ndipo Biliha anatenga pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna.

6. Rakele ndipo anati, Mulungu wandiweruzira ine, namva mau anga, nandipatsa ine mwana; cifukwa cace anamucha dzina lace Dani.

7. Ndipo Biliha mdzakazi wace wa Rakele anatenganso pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna waciwiri.

8. Ndipo Rakele anati, Ndi malimbano a Mulungu ndalimbana naye mkuru wanga, ndipo ndapambana naye; ndipo anamucha dzina lace Nafitali.

9. Pamene Leya anaona kuti analeka kubala, anatenga Zilipa mdzakazi wace, nampatsa iye kwa Yakobo kuti akhale mkazi wace.

Werengani mutu wathunthu Genesis 30