14. Ndipo anati Yehova Mulungu kwa njokayo, Cifukwa kuti wacita ici, wotembereredwa ndiwe wopambana ndi zinyama zonse ndi zamoyo zonse za m'thengo: uziyenda ndi pamimba pako, uzidya pfumbi masiku onse a moyo wako:
15. ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yace; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira citende cace.
16. Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzacurukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.
17. Kwa Adamu ndipo anati, Cifukwa kuti wamvera mau a mkazi wako, nudya za mtengo umene ndinakuuza iwe kuti, Usadyeko; nthaka ikhale yotembereredwa cifukwa ca iwe; m'kusauka udzadyako masiku onse a moyo wako:
18. minga ndi mitula idzakubalira iwe; ndipo udzadya therere la m'thengo:
19. m'thukuta la nkhope yako udzadya cakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: cifukwa kuti m'menemo unatengedwa: cifukwa kuti ndiwe pfumbi, ndi kupfumbiko udzabwerera.
20. Ndipo mwamuna anamucha dzina la mkazi wace, Hava; cifukwa ndiye amace wa amoyo onse.
21. Yehova Mulungu ndipo anapangira Adamu ndi mkazi wace maraya azikopa, nawabveka iwo.