Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 29:15-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo Labani anati kwa Yakobo, Cifukwa iwe ndiwe mbale wanga, kodi udzanditumikira ine kwacabe? Undiuze ine, malipiro ako adzakhala otani?

16. Ndipo Labani anali ndi ana akazi awiri, dzina la wamkuru ndi Leya, dzina la wamng'ono ndi Rakele.

17. Maso a Leya anali ofok a, koma Rakele anali wokoma thupi ndi wokongola.

18. Ndipo Yakobo anamkonda Rakele, nati, Ndidzakutumikirani inu zaka zisanu ndi ziwiri cifukwa ca Rakele mwana wanu wamkazi wamng'ono.

19. Ndipo anati Labani, Kuli kwabwino kuti ndimpatse iwe osampatsa kwa mwamuna wina; ukhalebe ndi ine.

20. Ndipo Yakobo anamtumikira zaka zisanu ndi ziwiri cifukwa ca Rakele; koma zidamuonekera iye ngati masiku owerengeka cifukwa ca cikondi cimene anamkonda iye naco.

21. Ndipo Yakobo anati kwa Labani, Undipatse Ine mkazi wanga, cifukwa masiku anga atha, kuti ndilowe kwa iye.

Werengani mutu wathunthu Genesis 29