Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 29:13-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo panali pamene Labani anamva mbiri ya Yakobo mwana wa mlongo wace, iye anathamangira kukakomana naye namfungatira, nampsompsona, namlowetsa m'nyumba mwace. Ndipo iye anamfotokozera Labani zinthu zonsezo.

14. Ndipo Labani anati kwa iye, Etu, iwe ndiwe pfupa langa ndi thupi langa. Ndipo anakhala naye nthawi ya mwezi umodzi.

15. Ndipo Labani anati kwa Yakobo, Cifukwa iwe ndiwe mbale wanga, kodi udzanditumikira ine kwacabe? Undiuze ine, malipiro ako adzakhala otani?

16. Ndipo Labani anali ndi ana akazi awiri, dzina la wamkuru ndi Leya, dzina la wamng'ono ndi Rakele.

17. Maso a Leya anali ofok a, koma Rakele anali wokoma thupi ndi wokongola.

18. Ndipo Yakobo anamkonda Rakele, nati, Ndidzakutumikirani inu zaka zisanu ndi ziwiri cifukwa ca Rakele mwana wanu wamkazi wamng'ono.

Werengani mutu wathunthu Genesis 29