Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 29:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yakobo ananka ulendo wace, nafika ku dziko la anthu a kum'mawa.

2. Ndipo anayang'ana, taonani, citsime m'dambo, ndipo, taonani, magulu atatu a nkhosa alinkugona kumeneko: pakuti pacitsimepo anamwetsa nkhosa; ndipo mwala wa pakamwa pa citsime unali waukuru.

3. Kumeneko ndipo zinasonkhana zoweta zonse: ndipo anagubuduza mwala kuucotsa pakamwa pa citsime, namwetsa nkhosa, naikanso mwala pakamwa pa citsime pamalo pace.

4. Ndipo anati Yakobo kwa iwo, Abale anga, ndinu a kuti inu? nati, Ndife a ku Harana.

5. Ndipo anati kwa iwo, Kodi mumdziwa Labani mwana wace wa Nahori? nati, Timdziwa.

6. Ndipo anati kwa iwo, Kodi ali bwino? nati, Ali bwino: taonani, Rakele mwana wace wamkazi alinkudza nazo nkhosa.

7. Ndipo iye anati, Taonani, kukali msana, si nthawi yosonkhanitsa zoweta; mwetsani nkhosa, pitani, kadyetseni.

8. Ndipo anati, Sitingathe, koma zitasonkhana ziweto zonse, ndipo atagubuduza mwala kuucotsa pakamwa pa citsime ndiko; pamenepo ndipo tizimwetsa nkhosa.

9. Ali cilankhulire nao, anafika Rakele ndi nkhosa za atate wace, cifukwa anaziweta.

10. Ndipo panali pamene Yakobo anaona Rakele, mwana wamkazi wa Labani, mlongo wace wa amace, ndi nkhosa za Labani mlongo wace wa amace, Yakobo anayandikira nagubuduza kuucotsa mwala pacitsime, nazimwetsa zoweta za Labani, mlongo wace wa amace.

11. Ndipo Yakobo anampsompsona Rakele nakweza mau ace, nalira.

12. Ndipo Yakobo anamuuza Rakele kuti iye ndiye mbalewace wa atate wace, kuti ndiye mwana wace wa Rebeka, ndipo Rakele anathamanga nakauza atate wace.

Werengani mutu wathunthu Genesis 29