Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 28:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Isake anamuitana Yakobo, namdalitsa iye, namuuza iye, nati kwa iye, Usatenge mkazi wa ana akazi a Kanani.

2. Tauka, nupite ku Padanaramu, ku nyumba ya Betuele, atate wa amai ako; ukadzitengere mkazi wa kumeneko kwa ana akazi a Labani mlongo wace wa amako.

3. Mulungu Wamphamvuyonse akudalitse iwe, akubalitse iwe, akucurukitse iwe, kuti ukhale khamu la anthu:

4. akupatse iwe mdalitso wa Abrahamu, iwe ndi mbeu zako pamodzi nawe: kuti ulowe m'dziko limene ukhalamo mlendo, limene Mulungu anampatsa Abrahamu.

5. Ndipo Isake anamlola Yakobo amuke, ndipo ananka ku Padanaramu kwa Labani, mwana wace wa Betuele Msuriya, mlongo wace wa Rebeka, amai wao wa Yakobo ndi Esau.

6. Ndipo anaona Esau kuti Isake anamdalitsa Yakobo namtumiza ku Padanaramu kuti atenge mkazi wa kumeneko;

7. ndiponso kuti pamene anamdalitsa iye, anamuuza iye kuti, Usatenge mkazi wa ana akazi a Kanani; ndiponso kuti Yakobo anamvera atate wace ndi amace, nanka ku Padanaramu;

8. ndipo Esau anaona kuti ana akazi a Kanani sanakondweretsa Isake atate wace:

9. ndipo ananka kwa Ismayeli, naonjezera kwa akazi amene anali nao, natenga Mahalati mwana wamkazi wa Ismayeli mwana wa Abrahamu, mlongo wace wa Nebayoti akhalemkazi wace.

10. Ndipo Yakobo anacoka m'Beereseba, nanka ku Harana.

11. Ndipo anafika kumalo, nagona kumeneko usiku, cifukwa lidalowa dzuwa: ndipo anatenga mwala wa kumeneko, nauika pansi pa mutu wace, nagona tulo kumeneko.

Werengani mutu wathunthu Genesis 28