Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 27:20-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndipo Isake anati kwa mwana wace, Unaipeza msanga bwanji mwana wanga? Ndipo anati, Cifukwa kuti Yehova Mulungu wanu anandiyendetsa ine bwino.

21. Ndipo Isake anati kwa Yakobo, Sendera kuno, ndikuyambase mwana wanga, ngati ndiwe mwana wanga Esau ndithu, kapena wina.

22. Ndipo Yakobo anasendera kwa Isake atate wace, ndipo anamyambasa nati, Mau ndi mau a Yakobo, koma manja ndi manja a Esau.

23. Ndipo sanazindikira iye, cifukwa kuti manja ace anali aubweya, onga manja a Esau mkuru wace; ndipo anamdalitsa iye.

24. Ndipo anati, Kodi ndiwe mwana wanga weniweni Esau? ndipo anati, Ndine amene.

25. Ndipo iye anati, Usendere nayo kwa ine, ndidye nyama ya mwana wanga, kuti moyo wanga ukudalitse iwe. Ndipo anasendera nayo kwa iye, nadya iye; ndipo anamtengera vinyo, namwa iye.

26. Ndipo Isake atate wace anati kwa iye, Senderatu, undimpsompsone mwana wanga.

27. Ndipo anasendera nampsompsona; ndipo anamva kununkhira kwa zobvala zace, namdalitsa, nati,Taona, kununkhira kwa mwana wanga,Kufanana ndi kununkhira kwa munda anaudalitsa Yehova;

28. Mlungu akupatse iwe mame a kumwamba,Ndi zonenepa za dziko lapansi,Ndi tirigu wambiri ndi vinyo;

29. Anthu akutumikire iwe,Mitundu ikuweramire iwe;Ucite ufumu pa abale ako,Ana a amako akuweramire iwe;Wotemberereka ali yense akutemberera iwe,Wodalitsika ali yense akudalitsa iwe.

30. Ndipo panali atatha Isake kumdalitsa Yakobo, ataturuka Yakobo pamaso pa Isake atate wace, Esau mkuru wace analowa kucokera kuthengo,

31. Ndipo iyenso anakonza cakudya cokolera, nadza naco kwa atate wace, nati kwa atate wace, Auke atate wanga, adye nyama ya mwana wace, kuti moyo wanu undidalitse ine.

32. Ndipo Isake atate wace anati kwa iye, Ndiwe yani? ndipo iye anati, Ndine mwana wanu woyamba Esau.

33. Ndipo Isake ananthunthumira ndi kunthunthumira kwakukuru, nati, Ndani uja anatenga nyama, nadza nayo kwa ine, ndipo ndadyako zonse usadaloweiwe, ndipondamdalitsaiye? inde, adzadalitsika.

34. Pamene Esau anamva mau a atate wace Isake, analira ndi kulira kwakukuru ndi kowawa kopambana, nati kwa atate wace, Mundidalitse ine, inenso atate wanga.

Werengani mutu wathunthu Genesis 27