Ndipo anasendera nampsompsona; ndipo anamva kununkhira kwa zobvala zace, namdalitsa, nati,Taona, kununkhira kwa mwana wanga,Kufanana ndi kununkhira kwa munda anaudalitsa Yehova;