Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 26:8-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo panali atakhala komwe masiku ambiri, Abimeleke mfumu ya Afilisti, anayang'ana kunja kwa zenera, napenya, taona, Isake analinkuseka ndi Rebeka mkazi wace.

9. Ndipo Abimeleke anamuitana Isake nati, Taona, uyo ndi mkazi wako ndithu: kodi bwanji unati, Ndiye mlongo wanga? Ndipo Isake anati kwa iye, Cifukwa ndinati, Ndingafe cifukwa ca iye.

10. Ndipo Abimeleke anati, Nciani cimeneci waticitira ife? panatsala pang'ono ena a anthu akadagona naye mkazi wako, ndipo ukadaticimwitsa ife:

11. Ndipo Abimeleke anauza anthu ace, nati, Ali yense amene akhudza mwamuna uyo kapena mkazi wace, zoonatu adzaphedwa.

12. Ndipo Isake anabzala m'dzikomo, nalandira za makumi khumi caka cimeneco; ndipo Yehova anamdalitsa iye.

13. Ndipo anakula munthuyo, nakulakula kufikira kuti anakhala wamkurukuru:

14. ndipo anali ndi cuma ca nkhosa, ndi cuma ca zoweta, ndi banja lalikuru: ndipo Afilisti anamcitira iye nsanje.

15. Ndipo zitsime zonse anakumba anyamata a atate wace Afilisti anazitseka, nazikwirira ndi dothi.

Werengani mutu wathunthu Genesis 26