Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 26:6-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo Isake anakhala m'Gerari;

7. ndipo anthu a kumeneko anamfunsa iye za mkazi wace; ndipo iye anati, diye mlongowanga: cifukwa kuti anaopa kunena, Mkazi wanga; anati, anthu a kumeneko angandiphe ine cifukwa ca Rebeka; popeza anali wokongola pakumuona.

8. Ndipo panali atakhala komwe masiku ambiri, Abimeleke mfumu ya Afilisti, anayang'ana kunja kwa zenera, napenya, taona, Isake analinkuseka ndi Rebeka mkazi wace.

9. Ndipo Abimeleke anamuitana Isake nati, Taona, uyo ndi mkazi wako ndithu: kodi bwanji unati, Ndiye mlongo wanga? Ndipo Isake anati kwa iye, Cifukwa ndinati, Ndingafe cifukwa ca iye.

10. Ndipo Abimeleke anati, Nciani cimeneci waticitira ife? panatsala pang'ono ena a anthu akadagona naye mkazi wako, ndipo ukadaticimwitsa ife:

11. Ndipo Abimeleke anauza anthu ace, nati, Ali yense amene akhudza mwamuna uyo kapena mkazi wace, zoonatu adzaphedwa.

Werengani mutu wathunthu Genesis 26