Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 25:7-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Masiku a zaka za moyo wace wa Abrahamu amene anakhala ndi moyo ndiwo zaka zana limodzi, kudza makumi asanu ndi limodzi, kudza khumi ndi zisanu.

8. Ndipo Abrahamu anamwalira, nafa m'ukalamba wace wabwino, nkhalamba ya zaka zambiri; natengedwa akhale ndi a mtundu wace.

9. Ndipo ana ace Isake ndi Ismayeli anamuika iye m'phanga la Makipela, m'munda wa Efroni mwana wace wa Zohari Mhiti, umene uli patsogolo pa Mamre;

10. munda umene anagula Abrahamu kwa ana a Heti: pamenepo anamuika Abrahamu ndi Sara mkazi wace.

11. Ndipo panali atafa Abrahamu, Mulungu anamdalitsa Isake mwana wace; ndipo Isake anakhala pa Beere-lahai-roi.

12. Mibadwo ya Ismayeli mwana wamwamuna wace wa Abrahamu, amene Hagara M-aigupto mdzakazi wa Sara anambalira Abrahamu ndi iyi:

13. ndipo maina a ana a Ismayeli, maina ao m'mibadwo yao ndi awa: woyamba wa Ismayeli ndi Nebayoti; ndi Kedara, ndi Abideele, ndi Mibisamu,

14. ndi Misima, ndi Duma; ndi Masa;

15. ndi Hadada, ndi Tema, ndi Yeturi, ndi Nafisi, ndi Kedema;

16. ana a Ismayeli ndi awa: maina ao m'midzi yao, m'misasa yao ndi awa: akaronga khumi ndi awiri m'mitundu yao.

17. Zaka za moyo wa Ismayeli ndi izi: zaka zana limodzi kudza makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri: ndipo iye anamwalira, natengedwa akhale ndi a mtundu wace.

Werengani mutu wathunthu Genesis 25