24. Atatha masiku ace akubala, taonani, amapasa anali m'mimba mwace.
25. Ndipo woyamba anabadwa wofiira, monse mwace monga maraya aubweya; ndipo anamucha dzina lace Esau.
26. Pambuyo pace ndipo anabadwa mphwace ndipo dzanja lace linagwira citende ca Esau, ndi dzina lace linachedwa Yakobo: ndipo Isake anali wa zaka makumi asanu ndi limodzi pamene mkazi wace anabala iwo.
27. Ndipo anakula anyamatawo; ndipo Esau anali munthu wakudziwa zakusaka nyama, munthu wa m'thengo; ndipo Yakobo anali munthu wofatsa, wakukhala m'mahema.
28. Ndipo Isake anakonda Esau, cifukwa anadya nyama yace ya m'thengo; koma Rebeka anakonda Yakobo,
29. Ndipo Yakobo anaphika mphodza: ndipo Esau anacokera kuthengo, nalefuka:
30. ndipo Esau anati kwa Yakobo, Undipatse ndidye cofiiraco; cifukwa ndalefuka: cifukwa cace anamucha dzina lace Edomu.
31. Ndipo Yakobo anati, Tigulane lero ukulu wako.
32. Ndipo Esau anati, Taona, ine ndifuna kufa: ukuluwo ndidzapindulanii nao?
33. Ndipo anati Yakobo, Undilumbirire ine lero lomwe, ndipo analumbirira iye; nagulana ndi Yakobo ukulu wace.
34. Ndipo Yakobo anampatsa Esau mkate ndi mphodza zophika; ndipo iye anadya, namwa, nanyamuka, napita; comweco Esau ananyoza ukulu wace.