Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 25:22-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo ana analimbana m'kati mwace: ndipo iye anati, Ngati cotero, ine ndikhala ndi moyo bwanji? ndipo ananka kukafunsa kwa Yehova.

23. Yehova ndipo anati kwa iye,Mitundu iwiri iri m'mimba mwako,Magulu awiri a anthu adzaturuka m'mimba mwako;Gulu lina lidzapambana mphamvu ndi linzace;Wamkuru adzakhala kapolo wa wamng'ono.

24. Atatha masiku ace akubala, taonani, amapasa anali m'mimba mwace.

25. Ndipo woyamba anabadwa wofiira, monse mwace monga maraya aubweya; ndipo anamucha dzina lace Esau.

26. Pambuyo pace ndipo anabadwa mphwace ndipo dzanja lace linagwira citende ca Esau, ndi dzina lace linachedwa Yakobo: ndipo Isake anali wa zaka makumi asanu ndi limodzi pamene mkazi wace anabala iwo.

27. Ndipo anakula anyamatawo; ndipo Esau anali munthu wakudziwa zakusaka nyama, munthu wa m'thengo; ndipo Yakobo anali munthu wofatsa, wakukhala m'mahema.

28. Ndipo Isake anakonda Esau, cifukwa anadya nyama yace ya m'thengo; koma Rebeka anakonda Yakobo,

29. Ndipo Yakobo anaphika mphodza: ndipo Esau anacokera kuthengo, nalefuka:

30. ndipo Esau anati kwa Yakobo, Undipatse ndidye cofiiraco; cifukwa ndalefuka: cifukwa cace anamucha dzina lace Edomu.

31. Ndipo Yakobo anati, Tigulane lero ukulu wako.

32. Ndipo Esau anati, Taona, ine ndifuna kufa: ukuluwo ndidzapindulanii nao?

33. Ndipo anati Yakobo, Undilumbirire ine lero lomwe, ndipo analumbirira iye; nagulana ndi Yakobo ukulu wace.

Werengani mutu wathunthu Genesis 25