Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 24:59-67 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

59. Ndipo anamlola Rebeka mlongo wao ndi mlezi wace, amuke pamodzi ndi mnyamata wace wa Abrahamu, ndi anthu ace.

60. Ndipo anamdalitsa Rebeka, nati kwa iye, Mlongo wathu ndiwe, iwe ukhale amai wa anthu zikwizikwi, mbeu zako zigonjetse cipata ca iwo akudana nao.

61. Ndipo adauka Rebeka ndi anamwali ace, nakwera pa ngamila natsata munthuyo: mnyamatayo ndipo anamtenga Rebeka namuka.

62. Ndipo Isake anadzera njira ya Beereahai-roi; cifukwa kuti anakhala iye n'dziko la kumwera.

63. Ndipo Isake anaturuka kulingalira m'munda madzulo; ndipo anatukula maso ace, nayang'ana, taona, ngamila zinalinkudza,

64. Ndipo Rebeka anatukula maso ace, ndipo pamene anaonalsake anatsika pa ngamila,

65. Ndipo anati kwa mnyamata, Munthuyo ndani amene ayenda m'munda kukomana ndi ife? Mnyamatayo ndipo anati, Uyo ndi mbuyanga: cifukwa cace namwali anatenga cophimba cace nadziphimba.

66. Mnyamatayo ndipo anamuuza Isake zonse anazicita.

67. Ndipo Isake anamlowetsa mkaziyo m'hema wa amace Sara, namtenga Rebeka, nakhala iye mkazi wace; ndipo anamkonda iye; ndipo Isake anatonthozedwa mtima atafa amace.

Werengani mutu wathunthu Genesis 24