Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 24:52-58 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

52. Ndipo panali pamene anamva mauwo mnyamata wa Abrahamu, anamgwadira Yehova pansi,

53. Ndipo mnyamatayo anaturutsa zokometsera zasiliva ndi zokometsera zagolidi, ndi zobvala, nampatsa Rebeka: ndipo anapatsa za mtengo wapatari kwa mlongo wace ndi amace.

54. Ndipo anadya namwa iye ndi anthu amene anali pamodzi naye, nagonapo usiku: ndipo anauka m'mamawa, ndipo iye anati, Mundilole ine ndinke kwa mbuyanga.

55. Ndipo mlongo wace ndi amace anati, Namwali akhale ndi ife masiku akuwerengeka, afikire khumi; patsogolo pace iye adzamuka.

56. Ndipo iye anati kwa iwo, Musandicedwetse ine, pakuti Yehova wandiyendetsa bwino m'njira yanga: mundilole ine ndinke kwa mbuyanga.

57. Ndipo anati iwo, Tidzamuitana namwaliyo, tidzamfunsa pakamwa pace.

58. Ndipo anamuitana Rebeka nati kwa iye, Kodi udzanka pamodzi ndi munthuyo? Ndipo anati, Ndidzanka.

Werengani mutu wathunthu Genesis 24