Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 24:13-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Taonani, ine ndiima pa citsime ca madzi; ndipo ana akazi a m'mudzi aturuka kudzatunga madzi;

14. ndipo pakhale kuti namwali amene ndidzati kwa iye, Tulatu mtsuko wako, ndimwe; ndipo iye adzati, Imwa, ndipo ndidzamwetsanso ngamila zako; yemweyo akhale mkazi wosankhira mnyamata wanu Isake; ndipo cotero ndidzadziwa kuti mwamcitira mbuyanga ufulu.

15. Ndipo panali, asanathe kunena, taonani, anaturuka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwace wa Abrahamu, ndi mtsuko wace paphewa pace.

16. Ndipo namwaliyo anali wokongola kwambiri m'maonekedwe ace, ndiye namwali wosamdziwa mwamuna, ndipo anatsikira kukasupe, nadzaza mtsuko wace, nakwera.

17. Ndipo mnyamatayo anamthamangira kukomana naye, nati, Ndimwetu madzi pang'ono a m'mtsuko mwako.

18. Ndipo anati, Imwa mbuyanga; nafulumira nayangata mtsuko m'manja mwace namwetsa iye.

19. Atatha kumwetsa iye, anati, Ndidzatungiranso ngamila zako, mpaka zitamwa zonse.

20. Ndipo anafulumira nathira madzi a m'mtsuko wace m'comwera, nathamangiranso kucitsime kukatunga, nazitungira ngamila zace zonse.

21. Munthuyo ndipo anamyang'anira iye, nakhala cete, kuti adziwe ngati Yehova anamuyendetsa bwino kapena iai.

22. Ndipo panali zitatha kumwa ngamila, munthuyo anatenga mphete yagolidi ya kulemera kwace sekele latheka, ndi zingwinjiri ziwiri za m'manja ace, kulemera kwace masekele khumi a golidi.

23. Ndipo anati, Ndiwe mwana wa yani? Undiuzetu. Kodi ku nyumba ya atate wako kuli malo akuti tigoneko ife?

24. Ndipo mkaziyo anati kwa iye, Ine ndine mwana wa Betuele mwana wamwamuna wa Milika, amene anambalira Nahori.

25. Natinso kwa iye, Tiri nao maudzu ndi zakudya zambiri oeli malo ogona.

Werengani mutu wathunthu Genesis 24