Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 23:7-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo anauka Abrahamu naweramira anthu a m'dzikomo, ana a Heti.

8. Ndipo ananena nao, kuti, Ngati mukandibvomereza kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso, mundimvere ine, mundinenere ine kwa Efroni mwana wace wa Zohari,

9. kuti andipatse ine phanga la Makipela, limene liri pansonga pa munda wace; pa mtengo wace wonse andipatse pakati pa inu, ndikhale nao manda.

10. Ndipo Efroni anakhala pakati pa ana a Heti: ndipo Efroni Mhiti anayankha Abrahamu alinkumva ana a Heti, onse amene analowa pa cipata ca mudzi wace, kuti,

11. Iai, mfumu, mundimvere ine; munda ndikupatsani inu, ndi phanga liri m'menemo ndikupatsani inu, pamaso pa ana a anthu anga ndikupatsani inu; ikani wakufa wanu.

12. Ndipo Abrahamu anawerama pamaso pa anthu a m'dzikomo.

13. Ndipo ananena kwa Efroni alinkumva anthu a m'dzikomo, kuti, Koma ngati ufuna, undimveretu ine: ndidzakupatsa iwe mtengo wace wa munda; uulandire kwa ine, ndipo ndidzaika wakufa wanga m'menemo.

14. Ndipo Efroni anamyankha Abrahamu, nati kwa iye,

Werengani mutu wathunthu Genesis 23