Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 23:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Sara anali wa zaka zana limodzi kudza makumi awiri ndi zisanu ndi ziwiri: ndizo zaka za moyo wa Sara.

2. Ndipo Sara anafa m'Kiriyati-araba (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani; ndipo Abrahamu anadza ku maliro a Sara, kuti amlire.

3. Ndipo Abrahamu anauka pa wakufa wace, nanena kwa ana a Heti, nati,

4. Ine ndine mlendo wakukhala ndi inu: mundipatse ndikhale ndi manda pamodzi ndi inu, kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso.

5. Ndipo ana a Heti anayankha Abrahamu nati kwa iye,

6. Mutimvere ife mfumu, ndinu karonga wamkuru pakati pa ife; muike wakufa wanu m'manda mwathu mosankhika: palibe munthu yense wa ife adzakaniza manda ace, kuti muike wakufa wanu.

7. Ndipo anauka Abrahamu naweramira anthu a m'dzikomo, ana a Heti.

8. Ndipo ananena nao, kuti, Ngati mukandibvomereza kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso, mundimvere ine, mundinenere ine kwa Efroni mwana wace wa Zohari,

9. kuti andipatse ine phanga la Makipela, limene liri pansonga pa munda wace; pa mtengo wace wonse andipatse pakati pa inu, ndikhale nao manda.

10. Ndipo Efroni anakhala pakati pa ana a Heti: ndipo Efroni Mhiti anayankha Abrahamu alinkumva ana a Heti, onse amene analowa pa cipata ca mudzi wace, kuti,

11. Iai, mfumu, mundimvere ine; munda ndikupatsani inu, ndi phanga liri m'menemo ndikupatsani inu, pamaso pa ana a anthu anga ndikupatsani inu; ikani wakufa wanu.

12. Ndipo Abrahamu anawerama pamaso pa anthu a m'dzikomo.

Werengani mutu wathunthu Genesis 23