Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 21:16-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo ananka nakhala pansi popenyana naye patari, monga pakugwa mubvi: cifukwa anati, Ndisaone kufa kwa mwana. Ndipo anakhala popenyana naye, nakweza mau ace nalira,

17. Ndipo Mulungu anamva mau a mnyamatayo, ndi mthenga wa Mulungu anamuitana Hagara, ndi mau odzera kumwamba, nati kwa iye, Watani Hagara? usaope; cifukwa Mulungu anamva mau a mnyamata kumene ali.

18. Tauka, nuukitse mnyamatayo, ndi kumgwira m'dzanja lako; cifukwa ndidzamuyesa iye mtundu waukuru.

19. Ndipo Mulungu anamtsegula m'maso mwace, ndipo anaona citsime ca madzi; namuka nadzaza mcenje ndi madzi, nampatsa mnyamata kuti amwe.

20. Ndipo Mulungu anakhala ndi mnyamata, ndipo anakula iye; nakhala m'cipululu, nakhala wauta.

21. Ndipo anakhala m'cipululu ca Parana; ndipo amace anamtengera iye mkazi wa ku dziko la Aigupto.

22. Ndipo panali nthawi yomweyo. Abimeleke ndi Fikolo kazembe wa nkhondo yace anati kwa Abrahamu, kuti, Mulungu ali pamodzi ndi iwe m'zonse uzicita iwe;

23. tsopano iwe undilumbirire ine pano pa Mulungu kuti sudzandinyenga ine, kapena mwana wanga, kapena mdzukulu wanga: koma monga ufulu ndakucitira iwe udzandicitire ine, ndi dziko lomwe wakhalamo, ngati mlendo.

24. Ndipo Abrahamu anati, Ine ndidzalumbira.

25. Ndipo Abrahamu anamdzudzula Abimeleke cifukwa ca citsime ca madzi, anyamata ace a Abimeleke anacilanda.

26. Ndipo anati Abimeleke, Sindinadziwe amene anacita ico; ndipo iwe sunandiuze ine, ndiponso sindinamve koma lero lino.

27. Ndipo Abrahamu anatenga nkhosa ndi ng'ombe, nampatsa Abimeleke, ndipo anapangana pangano onse awiriwo.

28. Ndipo Abrahamu anapatula ana a nkhosa akazi asanu ndi awiri pa okha.

29. Ndipo Abimeleke anati kwa Abrahamu, Nanga ana a nkhosa akazi asanu ndi awiri amene wapatula pa okha?

Werengani mutu wathunthu Genesis 21