14. Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi mcenje wa madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pace, ndi mwana, namcotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocerera m'cipululu ca Beereseba.
15. Ndipo anatha madzi a m'mcenje ndipo anaika mwana pansi pa citsamba.
16. Ndipo ananka nakhala pansi popenyana naye patari, monga pakugwa mubvi: cifukwa anati, Ndisaone kufa kwa mwana. Ndipo anakhala popenyana naye, nakweza mau ace nalira,
17. Ndipo Mulungu anamva mau a mnyamatayo, ndi mthenga wa Mulungu anamuitana Hagara, ndi mau odzera kumwamba, nati kwa iye, Watani Hagara? usaope; cifukwa Mulungu anamva mau a mnyamata kumene ali.
18. Tauka, nuukitse mnyamatayo, ndi kumgwira m'dzanja lako; cifukwa ndidzamuyesa iye mtundu waukuru.
19. Ndipo Mulungu anamtsegula m'maso mwace, ndipo anaona citsime ca madzi; namuka nadzaza mcenje ndi madzi, nampatsa mnyamata kuti amwe.
20. Ndipo Mulungu anakhala ndi mnyamata, ndipo anakula iye; nakhala m'cipululu, nakhala wauta.
21. Ndipo anakhala m'cipululu ca Parana; ndipo amace anamtengera iye mkazi wa ku dziko la Aigupto.