Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 20:3-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Koma Mulungu anadza kwa Abimeleke m'kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, cifukwa ca mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini.

4. Koma Abimeleke sanayandikire naye; ndipo anati, Ambuye, kodi mudzaphanso mtundu wolungama?

5. Kodi iye sanati kwa ine, Ndiye mlongo wanga: ndipo mkazi iye yekha anati, iye ndiye mlongo wanga: ndi mtima wanga wangwiro ndi manja anga osacimwa ndacita ine ici.

6. Ndipo Mulungu anati kwa iye m'kulota, lode ndidziwa ine, kuti wacita ico ndi mtima wangwiro, ndipo lnenso ndinakuletsa iwe kuti usandicimwire ine: cifukwa cace sindinakuloleza iwe kuti umkhudze mkaziyo.

7. Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wace; cifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nao.

8. Ndipo Abimeleke analawira m'mamawa, naitana anyamata ace onse, nanena zonse rimenezo m'makutu mwao, ndipo anthu anaopa kwambiri.

Werengani mutu wathunthu Genesis 20