Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 20:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Abrahamu ndipo anacoka kumeneko kunka ku dziko la kumwera, ndipo anakhala pakati pa Kedesi ndi Suri, ndipo anakhala ngati mlendo m'Gerari.

2. Ndipo Abrahamu anati za Sara mkazi wace, Iye ndiye mlongo wanga: ndipo Abimeleke mfumu ya Gerari anatumiza namtenga Sara.

3. Koma Mulungu anadza kwa Abimeleke m'kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, cifukwa ca mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini.

4. Koma Abimeleke sanayandikire naye; ndipo anati, Ambuye, kodi mudzaphanso mtundu wolungama?

5. Kodi iye sanati kwa ine, Ndiye mlongo wanga: ndipo mkazi iye yekha anati, iye ndiye mlongo wanga: ndi mtima wanga wangwiro ndi manja anga osacimwa ndacita ine ici.

6. Ndipo Mulungu anati kwa iye m'kulota, lode ndidziwa ine, kuti wacita ico ndi mtima wangwiro, ndipo lnenso ndinakuletsa iwe kuti usandicimwire ine: cifukwa cace sindinakuloleza iwe kuti umkhudze mkaziyo.

7. Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wace; cifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nao.

8. Ndipo Abimeleke analawira m'mamawa, naitana anyamata ace onse, nanena zonse rimenezo m'makutu mwao, ndipo anthu anaopa kwambiri.

9. Ndipo Abimeleke anaitana Abrahamu, nati kwa iye, Waticitira ife ciani iwe? Ndakucimwiranji iwe kuti waufikitsa pa ine ndi pa ufumu wanga ucimo waukuru? Wandicitira ine zosayenera kuzicita.

10. Ndipo Abimeleke anati kwa Abrahamu, Unaona ciani iwe kuti wacita ici?

Werengani mutu wathunthu Genesis 20