Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 19:12-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo anthu aja anati kwa Loti, Kodi muli nao ena pano? Mkamwini, ndi ana ako amuna, ndi ana ako akazi, ndi onse ali nao m'mudzi muno, uturuke nao m'malo muno:

13. popeza ife tidzaononga malo ano, cifukwa kulira kwao kwakula pamaso pa Yehova, ndipo Yehova anatitumiza ife kuti tiuononge.

14. Ndipo anaturuka Loti nanena nao akamwini ace amene anakwata ana ace akazi, nati, Taukani, turukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mudziwu; koma akamwini ace anamyesa wongoseka.

15. Pamene kunaca, amithengawo anafulumiza Loti, nati, Uka, tenga mkazi wako, ndi ana ako akazi awiri amene ali kunowa, kuti munganyeke m'mphulupulu ya mudzi.

16. Koma anacedwa; ndipo anthuwo anamgwira dzanja lace, ndi dzanja la mkazi wace ndi dzanja la ana ace akazi awiri; cifukwa ca kumcitira cifundo Yehova; ndipo anamturutsa iye, namuika kunja kwa mudzi.

17. Ndipo panali pamene anawaturutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usaceuke, usakhale pacigwa pali ponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke.

18. Ndipo Loti anati kwa iwo, Iaitu, mfumu;

19. taonanitu, kapolo wanu anapeza ufulu pamaso panu, ndipo munakuza cifundo canu, cimene munandicitira ine, pakupulumutsa moyo wanga; ine sindikhoza kuthawira kuphiri kuti cingandipeze ine coipaco ndingafe:

20. taonanitu, mudzi uwu uli pafupi pothawirapo, ndipo uli wong'ono; ndithawiretu kumeneko, suli wong'ono nanga? ndipo ndidzakhala ndi moyo.

21. Ndipo anati kwa iye, Taona, ndikubvomereza iwe pamenepanso kuti sindidzaononga mudzi uwu umene wandiuza.

22. Fulumira, thawira kumeneko; pakuti sindithai kucita kanthu usadafike kumeneko. Cifukwa cace anacha dzina la mudziwo Zoari.

23. Ndipo dzuwa lidakwera pa dziko pamene Loti anafika ku Zoari.

Werengani mutu wathunthu Genesis 19