Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 18:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova anamuonekera iye pa mtengo yathundu ya ku Mamre, pamene anakhala pa khomo la hema wace pakutentha dzuwa.

2. Ndipo anatukula maso ace, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pace; pamene anaona iwo, anawathamangira kucoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati,

3. Mbuyanga, ngatitu ndikapeza ufulu pamaso panu, musapitiriretu pa kapolo wanu;

4. nditengetu madzi pang'ono, ndikusambitseni mapazi anu, mupumule pansi pa mtengo;

5. ndipo ndidzatenga cakudya pang'ono, nimutonthoze mitima yanu; mutatero mudzapitirira, cifukwa mwafika kwa kapolo wanu. Ndipo anati, Cita comweco monga momwe wanena.

6. Ndipo Abrahamu analowa msanga m'hema wace kwa Sara, nati, Konza msanga miyeso itatu ya ufa wosalala, nuumbe, nupange mikate.

7. Ndipo Abrahamu anafulumira kunka kuzoweta, natenga kamwana ka ng'ombe kofewa ndi kabwino, napatsa mnyamata, ndipo anafulumira kuphika.

8. Ndipo anatenga mafuta amkaka, ndi mkaka, ndi kamwana ka ng'ombe kamene anaphika, naziika patsogolo pao; ndipo iye anaimirira iwo patsinde pa mtengo, ndipo anadya.

9. Ndipo anati kwa iye, Ali kuti Sara mkazi wako? Ndipo anati, Taonani m'hemamo.

10. Ndipo anati, Ndidzabwera kwa iwe ndithu pakufika nyengo yace; taonani Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna. Ndipo Sara anamva pakhomo pa hema amene anali pambuyo pace.

Werengani mutu wathunthu Genesis 18