Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 17:22-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo analeka kunena naye, ndipo Mulungu anakwera kucokera kwa Abrahamu.

23. Ndipo Abrahamu anatenga Ismayeli mwana wace ndi onse amene anabadwa m'nyumba mwace, ndi onse, amene anagulidwa ndi ndalama zace, amuna onse a mwa anthu a kunyumba kwace kwa Abrahamu, nadula khungu lao tsiku lomwelo, monga Mulungu ananena naye.

24. Ndipo Abrahamu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, pamene anadulidwa m'khungu lace.

25. Ndipo Ismayeli mwana wace anali wa zaka khumi ndi zitatu pamene anadulidwa m'khungu lace.

26. Tsiku lomwelo anadulidwa Abrahamu ndi Ismayeli mwana wace.

27. Ndipo amuna onse a m'nyumba mwace obadwa m'nyumba, ndi ogulidwa ndi ndalama kwa alendo, anadulidwa pamodzi naye.

Werengani mutu wathunthu Genesis 17