Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 17:21-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Koma pangano langa ndidzalimbikitsa ndi Isake, amene Sara adzakubalira iwe nthawi yomwe yino caka camawa.

22. Ndipo analeka kunena naye, ndipo Mulungu anakwera kucokera kwa Abrahamu.

23. Ndipo Abrahamu anatenga Ismayeli mwana wace ndi onse amene anabadwa m'nyumba mwace, ndi onse, amene anagulidwa ndi ndalama zace, amuna onse a mwa anthu a kunyumba kwace kwa Abrahamu, nadula khungu lao tsiku lomwelo, monga Mulungu ananena naye.

24. Ndipo Abrahamu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, pamene anadulidwa m'khungu lace.

25. Ndipo Ismayeli mwana wace anali wa zaka khumi ndi zitatu pamene anadulidwa m'khungu lace.

26. Tsiku lomwelo anadulidwa Abrahamu ndi Ismayeli mwana wace.

Werengani mutu wathunthu Genesis 17