Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 16:6-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Koma Abramu anati kwa Sarai, Taona, mdzakazi wako ali m'dzanja lako, umcitire iye cimene cikukomera m'maso mwako. Ndipo Sarai anamsautsa iye, ndipo anathawa kumaso kwace.

7. Ndipo mthenga wa Yehova anampeza iye pa kasupe wa madzi m'cipululu, pa kasupe wa pa njira ya ku Suri.

8. Ndipo anati, Hagara, mdzakazi wace wa Sarai, ufumira kuti? Unka kuti? Ndipo anati, Ndithawa ine kumaso kwace kwa wakuka wanga Sarai.

9. Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Bwera kwa wakuka wako, udzicepetse wekha pamanja pace.

10. Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Ndidzacurukitsa ndithu mbeu zako, kuti unyinji wao sudzawerengeka.

11. Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Taona, uli ndi pakati, ndipo udzabala mwana wamwamuna; nudzamucha dzina lace Ismayeli; cifukwa Yehova anamva kusauka kwako.

12. Ndipo iye adzakhala munthu wa m'thengo; ndipo dzanja lace lidzakhala lotsutsana ndi anthu onse, ndi manja a anthu onse adzakhala otsutsana naye: ndipo iye adzakhala pamaso pa abale ace onse.

13. Ndipo anacha dzina la Yehova amene ananena naye, Ndinu Mulungu wakundiona ine; pakuti anati, Kodi kunonso ndayang'ana pambuyo pace pa iye amene wakundiona ine?

14. Cifukwa cace citsimeco cinachedwa Beerelahai-roi; taonani ciri pakati pa Kadese ndi Berede.

Werengani mutu wathunthu Genesis 16