Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 15:2-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo Abramu anati, Ambuye Mulungu, mudzandipatsa ine ciani popeza ndine wopanda mwana, ndi amene adzakhala mwini nyumba yanga ndiye Eliezere wa ku Damasiko?

3. Ndipo Abramu anati, Taonani, simunandipatse ine mbeu; ndipo, taonani, wobadwa m'nyumba mwanga adzalowa m'malo mwanga.

4. Ndipo, taonani, mau a Yehova anadza kwa iye kuti, Uyu sadzakhala wakulowa m'malo mwako; koma iye amene adzaturuka m'cuuno mwako, ndiye adzakhala wakulowa m'malo mwako.

5. Ndipo anamturutsa iye kunja, nati, Tayang'anatu kumwamba, uwerenge nyenyezi, ngati ukhoza kuziwerenga zimenezo: ndipo anati kwa iye, Zoterezo zidzakhala mbeuzako.

6. Ndipo anakhulupirira Yehova, ndipo kunayesedwa kwa iye cilungamo.

7. Ndipo anatikwaiye, Ine ndine Yehova amene ndinaturutsa iwe m'Uri wa kwa Akaldayo, kuti ndikupatse iwe dziko limeneli likhale lako lako.

8. Ndipo anati, Ambuye Mulungu, nanga ndidzadziwa bwanji kuti lidzakhala colowa canga?

9. Ndipo anati kwa iye, Kanditengere Ine ng'ombe yaikazi ya zaka zitatu, ndi mbuzi yaikazi ya zaka zitatu, ndi tonde wa zaka zitatu, ndi njiwa, ndi bunda.

10. Ndipo anatenga iye zonse zimenezo, nazidula pakati, naika bandu popenyana ndi linzace: koma mbalame sanazidula.

11. Pamene miimba inatsikira panyama, Abramu anaingitsa iyo.

12. Ndipo linalinkulowa dzuwa, ndi tulo tatikuru tinamgwera Abramu: ndipo taonani, kuopsya kwa mdima waukuru kunamgwera iye.

13. Ndipo anati kwa Abramu, Dziwitsa ndithu kuti mbeu zako zidzakhala alendo m'dziko la eni, nizidzatumikira iwo, ndipo iwo adzasautsa izo zaka mazana anai;

14. ndiponso mtunduwo adzautumikira, Ine ndidzauweruza: ndiponso pambuyo pace adzaturuka ndi cuma cambiri.

Werengani mutu wathunthu Genesis 15