Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 15:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine cikopa cako ndi mphotho yako yaikurukuru.

2. Ndipo Abramu anati, Ambuye Mulungu, mudzandipatsa ine ciani popeza ndine wopanda mwana, ndi amene adzakhala mwini nyumba yanga ndiye Eliezere wa ku Damasiko?

3. Ndipo Abramu anati, Taonani, simunandipatse ine mbeu; ndipo, taonani, wobadwa m'nyumba mwanga adzalowa m'malo mwanga.

4. Ndipo, taonani, mau a Yehova anadza kwa iye kuti, Uyu sadzakhala wakulowa m'malo mwako; koma iye amene adzaturuka m'cuuno mwako, ndiye adzakhala wakulowa m'malo mwako.

5. Ndipo anamturutsa iye kunja, nati, Tayang'anatu kumwamba, uwerenge nyenyezi, ngati ukhoza kuziwerenga zimenezo: ndipo anati kwa iye, Zoterezo zidzakhala mbeuzako.

Werengani mutu wathunthu Genesis 15