Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 14:12-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo anagwira Loti mwana wa Abramu amene anakhala m'Sodomu, ndi cuma cace, namuka.

13. Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Mhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamre M-amori, mkuru wace wa Esakolo, ndi mkuru wace wa Aneri; amenewo ndiwo opangana naye Abramu.

14. Pamene anamva Abramu kuti mphwace anagwidwa, anaturuka natsogolera anyamata ace opangika, obadwa kunyumba kwace, mazana atatu kudza khumi ndi asanu ndi atatu, nawalondola kutikira ku Dani.

15. Ndipo anadzigawanizira iwo usiku, iye ndi anyamata ace, nawakantha, nawapitikitsa kufikira ku Hoba, ndiko ku dzanja lamanzere la ku Damasiko.

16. Ndipo anabwera naco cuma conse, nabwera naye Loti yemwe ndi cuma cace, ndi akazi ndi anthu omwe.

17. Ndipo anaturuka mfumu ya Sodomu kukomana naye, atabwera anatha kuwakantha Kedorelaomere ndi mafumu amene anali naye, ku cigwa ca Save (ndiko ku cigwa ca mfumu),

18. Ndipo Melikizedeke mfumu ya ku Salemu, anaturuka nao mkate ndi vinyo: iye ndiye wansembe wa Mulungu Wamkurukuru.

19. Ndipo anamdalitsa iye, nati, Abramu adalitsike ndi Mulungu Wamkurukuru, mwini kumwamba ndi dziko lapansi;

20. ayamikike Mulungu Wamkurukuru amene wapereka adani ako m'dzanja lako. Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse.

21. Mfumu ya Sodomu ndipo inati kwa Abramu, Ndipatse ine anthu, nutenge cuma iwe wekha.

22. Ndipo Abramu anati kwa mfumu ya Sodomu, Dzanja langa ndamtukulira Yehova, Mulungu Wamkurukuru, mwini kumwamba ndi dziko lapansi,

23. kuti sindidzatenga ngakhale thonje ngakhale cingwe ca nsapato, ngakhale kanthu kali konse kako, kuti unganene, Ndamlemeza Abramu;

Werengani mutu wathunthu Genesis 14