Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 12:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova anati kwa Abramu, Turuka iwe m'dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi ku nyumba ya atate wako, kunka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe;

2. ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukuru, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;

3. ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi,

4. Ndipo anamuka Abramu monga Yehova ananena kwa iye, ndipo Loti anamuka pamodzi naye: ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi awiri kudza zisanu, pamene anaturuka m'Harana.

5. Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wace, ndi Loti mwana wa mphwace, ndi cuma cao cimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala m'Harana; naturuka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani.

Werengani mutu wathunthu Genesis 12