Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 11:28-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Ndipo anafa Harana pamaso pa atate wace Tera m'dziko la kubadwa kwace, m'Uri wa kwa Akaldayo.

29. Ndipo Abramu ndi Nahori, anadzitengera okha akazi; dzina lace la mkazi wa Abramu ndilo Sarai; ndi dzina lace la mkazi wa Nahori ndilo Milika, mwana wace wa Harana, atate wace wa Milika, ndi atate wace wa Yisika.

30. Koma Sarai anali wouma; analibe mwana.

31. Ndipo Tera anatenga Abramu mwana wace wamwamuna, ndi Loti mwana wa Harana, mwana wace wamwamuna, ndi Sarai mpongozi wace, mkazi wa mwana wace Abramu; ndipo anaturuka pamodzi nao ku Uri wa kwa Akaldayo kuti amuke ku dziko la Kanani, ndipo anafika ku Harana, nakhala kumeneko.

32. Masiku a Tera anali zaka mazana awiri kudza zisanu; ndipo anafa Tera m'Harana.

Werengani mutu wathunthu Genesis 11