Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 11:10-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Mibadwo ya Semu ndi iyi: Semu anali wa zaka zana limodzi ndipo anabala Aripakasadi, citapita cigumula zaka ziwiri;

11. ndipo Semu anakhala ndi moyo zaka mazana asanu, atabala Aripakasadi, nabala ana amuna ndi akazi.

12. Ndipo Aripakasadi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza zisanu, nabala Sela;

13. ndipo Aripakasadi anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza zitatu, atabala Sela, nabala ana amuna ndi akazi.

14. Ndipo Sela anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala Ebere;

15. ndipo Sela anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza zitatu, atabala Ebere, nabala ana amuna ndi akazi.

16. Ndipo Ebere anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza zinai, nabala Pelege;

17. ndipo Ebere anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza makumi awiri, atabala Pelege, nabala ana amuna ndi akazi.

18. Ndipo Pelege anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala, Reu;

19. ndipo Pelege anakhala ndi moyo zaka mazana awiri kudza zisanu ndi zinai, atabala Reu, nabala ana amuna ndi akazi.

20. Ndipo Reu anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza ziwiri, nabala Serugi:

21. ndipo Reu anakhala ndi moyo zaka mazana awiri kudza zisanu ndi ziwiri, atabala Serugi, nabala ana amuna ndi akazi.

22. Ndipo Serugi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala Nahori:

23. ndipo Serugi anakhala ndi moyo zaka mazana awiri, atabala Nahori, nabala ana amuna ndi akazi.

24. Ndipo Nahori anakhala ndi moyo zaka makumi awiri kudza zisanu ndi zinai, nabala Tera:

25. ndipo ahori anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza khumi ndi zisanu ndi zinai, atabala Tera, nabala ana amuna ndi akazi.

26. Ndipo Tera anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi awiri, nabala Abramu, ndi Nahori ndi Harana.

27. Mibadwo ya Tera ndi iyi: Tera anabala Abramu, ndi Nahori, ndi Harana; ndipo Harana anabala Loti.

28. Ndipo anafa Harana pamaso pa atate wace Tera m'dziko la kubadwa kwace, m'Uri wa kwa Akaldayo.

29. Ndipo Abramu ndi Nahori, anadzitengera okha akazi; dzina lace la mkazi wa Abramu ndilo Sarai; ndi dzina lace la mkazi wa Nahori ndilo Milika, mwana wace wa Harana, atate wace wa Milika, ndi atate wace wa Yisika.

30. Koma Sarai anali wouma; analibe mwana.

Werengani mutu wathunthu Genesis 11