Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 7:8-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Katsala kamphindi, ndipo ndidzakutsanulira ukali wanga, ndi kukukwaniritsira mkwiyo wanga, ndi kukuweruza monga mwa njira zako, ndipo ndidzakubwezera zonyansa zako zonse.

9. Ndipo diso langa silidzalekerera, wosacita cifundo Ine, ndidzakubwezera monga mwa njira zako, ndi zonyansa zako zidzakhala pakati pako; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova wakukantha.

10. Taona, tsikuli, taona, lafika; tsoka lako laturuka, ndodo yaphuka mphundu za maluwa, kudzitama kwaphuka.

11. Ciwawa cauka cikhale ndodo ya coipa; sadzawatsalira ndi mmodzi yense, kapena wa unyinji wao, kapena wa cuma cao; sipadzakhalanso kuwalira maliro.

12. Yafika nthawi, layandikira tsikulo, wogula asakondwere, ndi wogulitsa asamve cisoni; pakuti mkwiyo ukhalira unyinji wao wense.

13. Pakuti wogulitsa sadzabwera ku cogulitsaco, cinkana akali ndi moyo, popeza masomphenyawo akunena unyinji wace wonse sadzapita pacabe, ndipo palibe mmodzi adzalimbitsa moyo wace m'mphulupulu yace.

14. Aomba lipenga, nakonzeratu zonse, koma palibe womuka kunkhondo; pakuti mkwiyo wanga ukhalira unyinji wace wonse.

15. Kunja kuli lupanga, ndi m'katimo muli mliri ndi njala; wokhala kuthenso adzafa ndi lupanga, ndi wokhala m'mudziyo njala ndi mliri zidzamutha.

16. Ndipo akupulumuka mwa iwo adzapulumuka, koma adzakhala kumapiri ngati njiwa za kuzigwa, onse akubuula, ali yense m'mphulupulu zace.

17. Manja onse adzalenda, ndi maondo onse adzaweyeseka ngati madzi.

18. Ndipo adzadzimangira m'cuuno ndi ziguduli, ndi zoopsetsa zidzawaphimba, ndi nkhope zonse zidzacita manyazi, ndi mitu yao yonse idzacita dazi.

19. Adzataya siliva wao kumakwalala, nadzayesa golidi wao cinthu codetsedwa; siliva wao ndi golidi wao sadzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova, sadzakwaniritsa moyo wao, kapena kudzaza matumbo ao; pakuti izi ndi cokhumudwitsa ca mphulupulu zao.

20. Ndipo cokometsera cace cokongola anaciyesa codzikuza naco, napanga naco mafanizo ao onyansa, ndi zonyansa zao zina; cifukwa cace ndinapatsa ici cikhale cowadetsa.

21. Ndipo ndidzacipereka m'dzanja la alendo cikhale colandika, ndi kwa oipa a m'dziko cikhale cofunkha; ndipo adzaciipsa.

22. Ndipo nkhope yanga idzawayang'anira kumbali, ndipo iwo adzadetsa pobisika panga, nadzalowamo acifwamba, nadzamudetsa.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 7