Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 7:19-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Adzataya siliva wao kumakwalala, nadzayesa golidi wao cinthu codetsedwa; siliva wao ndi golidi wao sadzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova, sadzakwaniritsa moyo wao, kapena kudzaza matumbo ao; pakuti izi ndi cokhumudwitsa ca mphulupulu zao.

20. Ndipo cokometsera cace cokongola anaciyesa codzikuza naco, napanga naco mafanizo ao onyansa, ndi zonyansa zao zina; cifukwa cace ndinapatsa ici cikhale cowadetsa.

21. Ndipo ndidzacipereka m'dzanja la alendo cikhale colandika, ndi kwa oipa a m'dziko cikhale cofunkha; ndipo adzaciipsa.

22. Ndipo nkhope yanga idzawayang'anira kumbali, ndipo iwo adzadetsa pobisika panga, nadzalowamo acifwamba, nadzamudetsa.

23. Sula unyolo, popeza dziko ladzala ndi mirandu yamwazi, ndi mudzi wadzala ndi ciwawa.

24. Cifukwa cace ndidzabwera nao amitundu oipitsitsa, ndipo iwo adzalandira nyumba zao ngati colowa, ndidzaleketsanso kudzikuza kwa amphamvu, kuti adetsedwe malo ao opatulika.

25. Cionongeko cirinkudza, adzafunafuna mtendere, koma palibe.

26. Lidzafika tsoka lotsatana-tsatana, kudzakhalanso mbiri yotsatana-tsatana, ndipo adzafunafuna masomphenya a mneneri, koma malamulo adzatayikira wansembe, uphungu ndi kutayikira akulu.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 7