Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 6:10-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, sindinanena cabe kuti ndidzawacitira coipa ici.

11. Atero Yehova Mulungu, Omba manja ako, ponda ndi phazi lako, nuti, Kalanga ine, cifukwa ca zonyansa zoipa zonse za nyumba ya Israyeli; pakuti adzagwa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri.

12. Wokhala kutali adzafa ndi mliri, wakhala pafupi adzagwa ndi lupanga; koma wotsala ndi kuzingidwa adzafa ndi njala; momwemo ndidzawakwaniritsira ukali wanga,

13. Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pokhala ophedwa ao pakati pa mafano ao, pozinga maguwa ao a nsembe, pa zitunda zonse zazitali, pamwamba pa mapiri onse, ndi patsinde pa mitengo yogudira yonse, ndi patsinde pa thundu ali yense wagudugudu, pomwe adapereka zonunkhira zokoma kwa mafano ao onse.

14. Ndipo ndidzawatambasulira dzanja langa, ndi kulisandutsa dziko bwinja ndi lopasuka, koposa cipululu ca ku Dibla mokhalamo iwo monse; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 6