Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 5:5-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Atero Yehova Mulungu, Uwu ndi Yerusalemu ndinauika pakati pa amitundu, ndi pozungulira pace pali maiko.

6. Koma anakaniza maweruzo anga ndi kucita zoipa koposa amitundu, nakaniza malemba anga koposa maiko akuuzungulira; pakuti anataya maweruzo anga, ndi malemba anga, sanayendamo.

7. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza kupokosera kwanu kwaposa kwa amitundu akukuzingani, ndipo simunayenda m'malemba anga, kapena kucita maweruzo anga, ngakhale maweruzo a amitundu akukuzingani simunawacita;

8. cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taona ndidzatsutsana nawe Inedi, ndi kucita maweruzo pakati pako pamaso pa amitundu.

9. Ndipo ndidzacita mwa iwe cimene sindinacicita ndi kale lonse, ndi kusadzacitanso momwemo, cifukwa ca zonyansa zako zonse.

10. Cifukwa cace atate adzadya ana pakati pako, ndi ana adzadya atate ao; ndipo ndidzacita maweruzo mwa iwe, ndi akutsala onse ndidzawabalalitsa ku mphepo zonse.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 5