Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 5:11-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. M'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, popeza wadetsa malo anga opatulika ndi zonyansa zako zonse ndi zoipsa zako zonse, ndidzakucepsa; diso langa silidzalekerera, ndi Inenso sindidzacita cifundo.

12. Limodzi la magawo atatu la iwe lidzafa ndi mliri, nilidzatha ndi njala pakati pa iwe; ndi limodzi lidzagwa ndi lupanga pozinga pako; ndi limodzi ndidzalibalalikitsa ku mphepo zonse, ndi kuwasololera lupanga lakuwatsata.

13. Motero mkwiyo wanga udzakwaniridwa, ndipo ndidzakhutitsa ukali wanga pa iwo, ndi kudzitonthoza; ndipo adzadziwa kuti Ine Yehova ndinanena m'cangu canga, pokwaniridwa nao ukali wanga.

14. Ndidzakuikanso ukhale bwinja ndi cotonza pakati pa amitundu akukuzinga, pamaso pa onse akupitirirapo.

15. Momwemo cidzakhala cotonza ndi mnyozo, cilangizo ndi codabwiza kwa amitundu akukuzinga, pamene ndikucitira maweruzo mu mkwiyo ndi ukali ndi madzudzulo aukali; Ine Yehovandanena.

16. Pakuwatumizira Ine mibvi yoipa ya njala yakuononga, imene ndidzatumiza kukuonongani, pamenepo ndidzakukuzirani njala, ndi kukutyolerani mcirikizo, ndiwo cakudya.

17. Inde ndidzakutumizirani njala ndi zirombo, ndipo zidzakusowetsa ana ako; ndi mliri ndi mwazi zidzakugwera; ndidzakufikitsiranso lupanga; Ine Yehova ndacinena.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 5